The Maravi Post

Switch to desktop Register Login



Chavula zavuta ku Lebanon

Moses-ChavulaBLANTYRE--Kaputeni wongogwirizira wa timu ya Flames, Moses Chavula, wabwereranso ku South Africa kuchokera ku Lebanon komwe adapita kuti akayesere mwawi wosewera mpira kumeneko koma zidakanika zitayang’anana.

Chavula adauza nyuzipepala ya The Nation kuchokera ku South Africa kuti poyamba adayenera kukayesa mwawi wake ndi timu yotchedwa Chabab Al Sahel koma manijala wake adamuuza akufuna wotchinga kumbuyo koma pakati osati kumanzere.
“
Kenaka ndidapita ku timu ya Nejmeh SC komwe ndidachita nawo tirening’i tsiku limodzi lokha chifukwa nawonso amafuna wotchinga kumbuyo chapakati,” adatero Chavula.

Mnyamatayu adati zonsezo zidachitika chifukwa padali kusamvetsetsana pakati pa manijala wake ndi matimu awiriwo.

Iye adati kukukhala ngati makalabuwo adauza manijala wake kuti akufuna madifenda koma sadatchule kuti akufuna difenda wanji.
“
Pachifukwa ichi ndidangoganiza zobwerera Ku Durban,” adatero Chavula. Akuti mwawi udakalipobe woti akhoza kupeza timu ina ndipo sakutaya mtima chifukwa cha mawu aja oti “ukasauka sunga khosi mkanda woyera udzavala”.

Chavula, yemwe wakhala akusewera mpira m’timu ya Amazulu, adagwirizana ndi eni timuyo kuti asiyanepo atalepherana Chichewa pakutha kwa sizoni yapitayi makamaka chifukwa amangomusunga pabenchi nthawi zambiri, osamuseweretsa mpira monga iye ankafunira.

Iyeyutu adaoita ku Joniko m’chaka cha 2008 ndipo asayina mgwirizano wosewera mpira m’timu ya Nathi Lions kwa zaka zitatu. Kenako mpamene amalowa timu ya Amazulu komwe zinthu sizidayendeko.

Amalawi ambiri sizikuwayendera ku Joniko masiku ano ndipo ambiri akuganiza zongobwerera kumudzi.
Tikuyankhula pano osewewera mpira monga Fischer Kondowe, Joseph Kamwendo, Dave Banda, Sankhani Mkandawire, Swadik Sanudi, Grant Lungu ndi ena adabwerera kumudzi ndipo akusewera mu Supa Ligi.    
Koma Peter Wadadwa wasemphana nacho chipululachi chifukwa asewerabe komweko m’timu ya Thanda Royal Zulu limodzi ndi Mmalawi winanso, Jimmy Zakazaka.

Enanso amene zikukhala ngati zikuwayendera ndi Robert Ng’ambi, Robin Ngalande ndi Atusaye Nyondo.



@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version