The Maravi Post

Switch to desktop Register LoginWantchito apha bwana wake

BLANTYRE--Zoopsa anthuni! Wantchito wina ku Soche East mumzinda wa Blantyre wapha bwana wake ndi kumukwirira m’nkhuti ya zinyalala kenaka n’kumubera galimoto yake.

Thupi la bwana wophedwayo, yemwe dzina lake ndi Richard Nsamala, wazaka 51 ndipo ankagwira ntchcito ku Indebank mumzinda wa Blantyre womwewo, adaufukula m’manda osayenerawo Lachitatu ndipo anthu miyandamiyanda adabwera kudzachitira umboni zoopsazo mmene apolisi amafukula mtembowo.

Mkulu wa CID ku Blantyre, Bob Mtekama, adauza Maravi Post kuti watchitoyo, yemwe dzina lake ndi Timothy Sinalo ndipo ali ndi zaka 26 ndipo amagwira ntchito yam’nyumba, adapotokola khosi bwana wakeyo mothandizana ndi Kenneth Chimwanga pakati pa usiku wa Loweruka ndi Lamulungu lapitali.

Atatero adakwirira mtembo wa Nsamala m’nkhuti yazinyalala mkati mwa mpanda wa nyumba yake yomweyo ndipo adaba galimoto ndi kukaibisa m’mudzi wina kwa Bvumbwe, m’boma la Thyolo.

Koma magazi a munthu ngoopsa. Mfumu Bvumbwe ya ku Thyolo idadabwa ndi galimotolo m’mudzi mwake ndipo idabentulira apolisi kwa Bvumbwe ndipo apolisiwo adathamangira komweko nakambwandira anthu anayi amene adapezeka pafupi ndi galimoto yobedwayo yamtundu wa Toyota Marino.

Pambuyo pake atapanikizidwa, Sinalo, yemwe poyamba adati ndi mbale wake wa Nsamala, adavomera kuti amanama pamene mkulu wake weniweni wa Nsamala, yemwe dzina lake ndi Martin, atamukana poyera kuti sakumudziwa ndipo palibe chibale ndi iye. Sinalo kenaka adanamanso kuti Nsamala adapita kwawo ku Nsanje.

Mkulu wa CID uja adati anthu anayiwo adapita nawo ku Polisi ya Soche komwe atawapana nawo mafunso adati Sinalo adavomera kuti adaphadi bwana wake mothandizana ndi mnzake ndipo adawalozera pomwe adakwirira mtembo wake.

Khwimbi la anthu lidasonkhana ku Soche East dzulo kuchitira umboni pomwe apolisi ankafukula mtembo wa Nsamala.


@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version