Written by MTOLANKHANI WATHU
LILONGWE--Ganizo la chipani cholamula cha People’s Party (PP) lothetsa ndi kukhazikitsanso kachiwiri makomiti achitukuko cha kumidzi autsa mapiri pachigwa pomwe mafumu ambiri m’boma la Thyolo sakugwirizana ndi ganizoli ndipo atsindika kuti sadzagwira ntchito ndi makomiti atsopanowa.
Akuluakulu a chipani cha PP akhala ali pakalikiliki “kuthetsa ndi kukonzanso” ma Area Development Committee (ADC), Village Development Committee (VDC) ndi cholinga choti aikemo anthu awo otsatira chipanichi mumakomitiwa.
Ena mwa makomiti amene athetsedwa kale ndi Nchilamwela VDC, Nanseta ADC, Bvumbwe ADC ndi Kapichi ADC.
Koma izi zakwiyitsa mafumu m’bomali omwe akuwona ngati boma likufuna kugwiritsa ntchito makomiti atsopanowa pofuna kukwaniritsa zofuna zake pandale komanso kuthana ndi omwe satsatira chipanichi.
Polankhula ndi mtolankhani wa Maravi Post ku Khonjeni m’boma la Thyolo atangomaliza kuphwasula komiti yakale ndi kukhazikitsa komiti yatsopano ya Kapichi ADC, gavinala wa chipani cha PP m’boma la Thyolo (district governor) Andrew Chipote anati makomiti akale amasowa chilungamo pakagwiridwe kawo ka ntchito n’kuwona chipani cha PP chaganiza zokhazikitsa makomiti omwe angagwire ntchito mokhulupirika.
Iwo anati chipani chawo chimakhulupirira kuti chilungamo chizikhala patsogolo pantchito za chitukuko pofuna kuti chitukuko chifikire Mmalawi aliyense.
“Izo ndi zoona! Kuyamba pa 17 Seputembala, ine ndi komiti yanga takhala tikunka tikonza makomiti a VDC, ADC komanso ma Community-Based Organisations (CBOs) ndi cholinga choti nafenso a PP tikhale ndi otiyimira m’makomiti amenewa. Vuto ndi loti, mmbuyo monsemu, makomitiwa amadzadza ndi otsatira DPP okha; ndipo ankakonderana pakabwera zabwino kuchoka kuboma kumasiya ena akungovutika,” anatero a Chipote.
Iwo anatchula ntchito za Public Works ndi feteleza wa makuponi ngati zina mwa ntchito zimene akuti makomiti akale ankakonderana polembana maina a wanthu a chipani chimodzi.
“Koma tikakhala ndi nthumwi zathu m’makomiti amenewa, nkhani zosankhirana sidzakhalanso chifukwa mbali ziwirizi zidzatha kumagawana mwachilungamo zimene zilipo monga feteleza wa makuponi,” anatero a Chipote.
Koma imodzi mwa mafumu odziwika bwino m’bom la Thyolo Inkosi Bvumbwe yati iyo ikukayika ngati cholinga chenicheni chothetsera makomiti akale ndiye kupititsa patsogolo ntchito za makomitiwa.
Bvumbwe akuti makomiti achitukuko amayenera kukhala oyima paokha ndipo sayenera kutengapo gawo lalikulu pa ndale kupatula kuponya voti.
“Makomiti a ADC, VDC ndi CBO ndi achitukuko. Choncho, akuyenera kukhala oyima paokha. Ndiye chimene akufuna a PP ndi chiyani chifukwa awa si makomiti a chipani kuti aziti nafenso tikhale ndi nthumwi zathu m’menemu?” idafunsa Inkosi Bvumbwe.
“Pempho langa ndi lakuti ngati pali wandale aliyense amene akufuna kudzakhazikitsa maziko a chipani chake kuno, angobwera. Khomo ndi lotsekuka. Abwere adzatipeza, koma zoti azisokoneza makomiti achitukuko m’dzina lokonza zinthu si bwino,” inadaonjeza motero mfumuyi.