The Maravi Post

Switch to desktop Register LoginKuphedwa kwa Chasowa: Masangwi ndi ena asanu anjatidwa

Masangwi (Pakati) mmene amafika ku Polisi ya Chichiri atatsagana ndi Kaphale (Kumanzere) ndi Mulli. BLANTYRE: Zayambikatu! Pamene boma likupitiriza kufufuza za imfa ya Robert Chasowa yemwe adali m’chaka chomaliza pasukulu yaukachenjede ya Malawi Polytechnic apolisi mumzinda wa Blantyre akwidzinga unyolo gavinala wa chigawo chakumwera wa chipani chakale cholamulira cha Democratic Progressive Party (DPP) Noel Masangwi ndi ena asanu kuti akayankhe mlandu powaganizira kuti adatengapo mbali pachiwembucho.Masangwi anakadzipereka okha kumaofesi a likulu la Polisi m’chigawo chakumwera ku Chichiri nthawi ya 9 koloko m’mawa Lachitatu apolisi atasiya uthenga kunyumba kwawo ku Kanjedwa kuti akufunika kupolisi. Adatsagana ndi womuyira pa mlanduwu, Kalekeni Kaphale, achibale ndi ena omufunira zambwino monga Feston Mulli, yemwe ndi wabizinesi wotchuka kwambiri m’dziko la Malawi.

Mneneri wa apolisi m’chigawo chakumwera Nicholas Gondwa wauza Maravipost kuti Lachiwiri pa Okutobala 23 chakumbandakucha adamanganso wapolisi Stanford Horea, wotukula masewero ankhonya Mike Chitenje, mkulu wa achinyamata m’chipani cha DPP Louis Ngalande, Stone Mwamande ndi Sam Chulu.

Gondwa adachenjeza kuti ena ambiri okhudzidwa ndi imfa ya Chasowa ali pamndandanda woti athiridwe unyolo.
Chasowa adapezeka atamwalira mwadzidzidzi pa 24 Seputembala chaka chathachi pasukulupo pamene apolisi adati wachita kudzipha podziponya pasimenti kuchokera pamwamba pa nyumba zogona (mahositelo). Koma malinga ndi mmene zinthu zidalili panthawiyo, zidaoneka kuti pali bii pali munga—mnyamatayo adachita chobaya!

Pulezidenti Joyce Banda adakhazikitsa komiti ya akatakwe oti afufuze za imfa ya Chasowa atangokhala pampando wa utsogoleri wa dziko lino Bingu wa Mutharika atatsamira mkono mwezi wa Epulo chaka chonchino.

M’kafukufuku wawo, komitiyi idapeza kuti Chasowa adachitadi kuphedwa osati kudziphedwa monga adanenera apolisi poyamba ndipo m’lipoti lawo adatchulapo maina a anthu angapo amene akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa mnyamatayo, yemwe adali m’chaka chotsiriza cha maphunziro ake a Engineering.Tags: Noel Masangwi  

@2010 The Maravi Post an Eltas EnterPrises INC Publishing Company
Site Developed By JRC

Top Desktop version